Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

January 6-12

MASALIMO 127-134

January 6-12

Nyimbo Na. 134 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Makolo, Pitirizani Kusamalira Cholowa Chanu Chamtengo Wapatali

(10 min.)

Makolo akhoza kudalira Yehova kuti awathandiza kupezera banja lawo zofunika pa moyo (Sl 127:1, 2)

Ana ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Yehova (Sl 127:3; w21.08 5 ¶9)

Muziphunzitsa mwana aliyense mogwirizana ndi zimene amafunikira (Sl 127:4; w19.12 27 ¶20)

Yehova amasangalala ngati makolo amamudalira komanso amayesetsa kuchita zonse zomwe angathe posamalira ana awo

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 128:3—N’chifukwa chiyani wolemba masalimo anayerekezera ana ndi mphukira za mtengo wa maolivi? (it-1 543)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. (lmd phunziro 1 mfundo 3)

5. Ulendo Woyamba

(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Munthuyo watchula zimene amakhulupirira koma ndi zotsutsana ndi zimene Baibulo limaphunzitsa. (lmd phunziro 5 mfundo 4)

6. Kuphunzitsa Anthu

(5 min.) lff phunziro 16 mfundo 4-5. Konzani zoti wophunzira wanuyo adzaphunzire Baibulo ngakhale kuti inu mukuchokapo. (lmd phunziro 10 mfundo 4)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 13

7. Makolo, Kodi Ndinu Chitsanzo Chabwino kwa Ana Anu?

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Gulu la Yehova latulutsa zinthu zambiri pofuna kuthandiza makolo kuti aziphunzitsa ana awo zokhudza Yehova. Komabe, njira yabwino kwambiri imene makolo angagwiritse ntchito ndi chitsanzo chawo chabwino.—De 6:5-9.

Yesu ankagwiritsa ntchito njira imeneyi pophunzitsa ophunzira ake.

Werengani Yohane 13:13-15. Kenako funsani omvera funso ili:

  • N’chifukwa chiyani mukuganiza kuti njira imene Yesu ankagwiritsira ntchitoyi inali yothandiza kwambiri?

Monga makolo, zimene mumachita zingathandize ana anu kumvetsa kuti zimene mumawaphunzitsa ndi zoona. Chitsanzo chanu chabwino chikhozanso kuwathandiza kuti azilemekezeka zimene mumawaphunzitsa komanso azikumverani mosavuta.

Onerani VIDIYO yakuti Ana Athu Anatengera Chitsanzo Chathu. Kenako funsani omvera mafunso otsatirawa:

  • Kodi M’bale ndi Mlongo Garcia anaphunzitsa ana awo zinthu zofunika ziti?

  • Kodi vidiyoyi yakulimbikitsani bwanji kuti mupitirizebe kukhala chitsanzo chabwino kwa ana anu?

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 20 ¶13-20

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 73 ndi Pemphero