MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Mungachite Upainiya kwa Chaka Chimodzi?
Kodi mungapeze madalitso otani ngati mutachita upainiya?
MUKAMACHITA UPAINIYA, MUKHOZA KUPEZA MADALITSO OTSATIRAWA:
-
Mukhoza kukhala ndi luso lolalikira ndipo mungamasangalale mu utumiki.
-
Mungamakonde kwambiri Yehova. Mukamauza ena zokhudza Yehova m’pamenenso mumaganizira kwambiri za makhalidwe ake abwino.
-
Mungaone ubwino woika zinthu za Ufumu pamalo oyamba m’malo mwa zofuna zanu. Mungakhalenso osangalala mukamagwiritsa ntchito nthawi komanso zinthu zanu pothandiza ena mu utumiki.
—Mat. 6:33; Mac. 20:35 -
Mukhoza kulowa Sukulu ya Apainiya, kuchita nawo msonkhano wa apainiya womwe umachitika msonkhano wadera ukayandikira komanso womwe woyang’anira dera amachititsa akamachezera mpingo.
-
Mungapeze anthu ambiri oti muziphunzira nawo Baibulo.
-
Mungamakhale nthawi yaitali muli ndi abale ndi alongo, omwe angakulimbikitseni komanso kukuthandizani.
—Aroma 1:11, 12