Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

July 16-22

Luka 10-11

July 16-22

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

  • Fanizo la Msamariya Wachifundo”: (10 min.)

    • Luka 10:29-32​—Wansembe komanso Mlevi analephera kuthandiza Myuda yemwe anamenyedwa ndi achifwamba [Onetsani “Msewu Wochoka ku Yerusalemu Kupita ku Yeriko” zithunzi ndi mavidiyo pa Luka 10:30, nwtsty.] (w02 9/1 16-17 ¶14-15)

    • Luka 10:33-35​—Msamariya anasonyeza chikondi chachikulu kwa munthu amene anamenyedwa ndi achifwamba (“Msamariya wina” “anamanga komanso kuthira mafuta ndi vinyo m’mabalamo” “kunyumba ya alendo” mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 10:33, 34, nwtsty)

    • Luka 10:36, 37​—Tiyenera kumakonda anthu onse, osati anthu amaphunziro, mtundu kapena fuko lathu okha (w98 7/1 31 ¶2)

  • Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)

    • Luka 10:18​—Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene anauza ophunzira ake 70 kuti: “Ndinayamba kuona Satana atagwa kale ngati mphezi kuchokera kumwamba”? (“Ndinayamba kuona Satana atagwa kale ngati mphezi kuchokera kumwamba”mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 10:18, nwtsty; w08 3/15 31 ¶11)

    • Luka 11:5-9​—Kodi fanizo la munthu yemwe sanasiye kupempha likutiphunzitsa chiyani pa nkhani ya pemphero? (“Bwanawe, ndibwerekeko mitanda itatu ya mkate” “Usandivutitse ine” “chifukwa cha kukakamira kwake” mfundo zimene ndikuphunzira pa Luka 11:5-9, nwtsty)

    • Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

    • Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

  • Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Luka 10:1-16

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

  • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Yambani ndi chitsanzo cha zimene tinganene. Sonyezani mmene mungayankhire pa nkhani inayake yomwe anthu a m’gawo lanu amatsutsa kawirikawiri.

  • Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha zimene tinganene. Sonyezani zimene mungachite ngati munthu amene mwamupeza wanena kuti akudya.

  • Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Wachiwiri: (5 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU