KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI
Muzisonyeza Kuti Mumawaganizira
Kuganizira ena kumatanthauza kumvetsa mmene akumvera, zomwe akuganiza, mfundo zimene amayendera komanso zomwe akufunikira. Timasonyeza kuti timaganizira ena ngati tili ndi mtima wofuna kuwathandiza ndipo anthuwo savutika kuzindikira kuti timawaganizira. Tikamaganizira ena mu utumiki, timasonyeza kuti tikutsanzira Yehova yemwe ndi wachikondi komanso amaganizira anthu, ndipo zimenezi zimachititsa anthuwo kufuna kudziwa zambiri zokhudza Yehovayo.—Afi 2:4.
Kuganizira ena sikuti yangokhala njira imene timagwiritsa ntchito tikakhala mu utumiki. Koma timasonyeza kuti timaganizira ena tikamawamvetsera mwatcheru, tikamawalankhula mokoma mtima, tikakhala ndi maganizo oyenera, komanso tikamagwiritsa ntchito manja ndi nkhope yathu moyenera. Timasonyeza kuti timaganizira ena tikamachita nawo chidwi. Tiyenera kudziwa zimene amakonda, zimene amakhulupirira komanso mmene zinthu zilili pamoyo wawo. Tiyeneranso kuwapatsa mfundo zomwe zingawathandize, koma tisawakakamize kuti asinthe. Anthu omwe tikuwalalikira akalola kuti tiwathandize, timasangalala kwambiri ndi utumiki.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIWONJEZERA LUSO LANU KUTI MUZISANGALALA NDI NTCHITO YOPHUNZITSA—MUZISONYEZA KUTI MUMAWAGANIZIRA, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Jane atachedwa ku phunziro, kodi Anita anasonyeza bwanji kuti amamuganizira?
-
Jane atanena kuti wapanikizika moti sakwanitsa kuphunzira, kodi Anita anasonyeza bwanji kuti amamuganizira?
-
Jane atanena kuti sachita zinthu mwadongosolo, kodi Anita anasonyeza bwanji kuti amamuganizira?