MOYO WATHU WACHIKHRISTU | MUKHALE NDI ZOLINGA MU CHAKA CHAUTUMIKI CHIKUBWERACHI
Mukhale ndi Zolinga mu Chaka Chautumiki Chikubwerachi—Funsirani Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu
Kuti munthu alowe Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu (SKE), sachita kufunika kukhala wapadera. Zomwe zimafunika kwambiri ndi kukhala munthu wauzimu komanso kukhala wofunitsitsa kulandira utumiki uliwonse kuchokera m’gulu la Yehova.—Yes 6:8.
ONERANI VIDIYO YAKUTI LOWANI PA KHOMO LA UTUMIKI MWACHIKHULUPIRIRO—FUNSIRANI SUKULU YA AKHRISTU OLALIKIRA ZA UFUMU, KENAKO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:
-
N’chifukwa chiyani Gabriel ankazengereza kufunsira sukulu ya SKE, nanga kuganizira mozama lemba la Afilipi 4:13 kunamuthandiza bwanji?