Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU | MUKHALE NDI ZOLINGA MU CHAKA CHAUTUMIKI CHIKUBWERACHI

Mukhale ndi Zolinga mu Chaka Chautumiki Chikubwerachi​—Thandizani pa Ntchito Yazomangamanga

Mukhale ndi Zolinga mu Chaka Chautumiki Chikubwerachi​—Thandizani pa Ntchito Yazomangamanga

Utumiki womanga malo amene amagwiritsidwa ntchito polambira Yehova ndi wapadera. (Eks 36:1) Kodi nthawi zina mungamathandize nawo pa ntchito zomangamanga zimene zikuchitika pafupi ndi kwanu? Ngati ndi choncho, mungalembe Fomu ya Wofuna Kutumikira Mongodzipereka M’dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga (DC-50). Kapena kodi mungadzipereke kwa mawiki kapena miyezi ingapo kuti mukathandize nawo pa ntchito zimene zikuchitikira kutali? Ngati ndi choncho, mungalembe Fomu ya Amene Akufuna Utumiki Wongodzipereka (A-19). Munthu sachita kufunika kukhala ndi luso la zomangamanga kuti athandize nawo pantchitoyi.​—Ne 2:1, 4, 5.

ONERANI VIDIYO YAKUTI LOWANI PA KHOMO LA UTUMIKI MWACHIKHULUPIRIRO​—THANDIZANI PA NTCHITO YAZOMANGAMANGA, KENAKO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:

  • Kodi Sarah ankadera nkhawa za chiyani, nanga n’chiyani chinamuthandiza?