CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Anagwira Ntchito Mwamphamvu Komanso ndi Mtima Wonse
Solomo anagwiritsa ntchito zinthu zabwino kwambiri pomanga kachisi (1Mf 5:6, 17; w11 2/1 15)
Aisiraeli ambiri anagwira nawo ntchitoyi (1Mf 5:13-16; it-1 424; it-2 1077 ¶1)
Solomo ndi Aisiraeli anagwira mwakhama ntchitoyi kwa zaka 7 (1Mf 6:38; onani chithunzi chapachikuto)
Solomo ndi Aisiraeli anakwanitsa kumanga kachisi wokongola woti azilambiriramo Yehova chifukwa chakuti ankamukonda kwambiri. Koma n’zomvetsa chisoni kuti mibadwo imene inabwera pambuyo pawo, inasiya kulambira Yehova ndi mtima wonse. Iwo anasiya kusamalira kachisi ndipo kenako kachisiyo anawonongedwa.
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndikuchita zotani kuti ndipitirizebe kulambira Yehova ndi mtima wonse?’