Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Ntchito Yapadera Yoyambitsa Maphunziro a Baibulo mu September

Ntchito Yapadera Yoyambitsa Maphunziro a Baibulo mu September

M’mwezi wa September, tidzagwira mwakhama ntchito yapadera yoyambitsa maphunziro a Baibulo ku nyumba ndi nyumba pogwiritsa ntchito kabuku kakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Ofalitsa angasankhe kudzachita upainiya wothandiza wa maola 30. Kodi tidzagwira bwanji ntchito yapaderayi?

  • Pa Ulendo Woyamba: Gwiritsani ntchito tsamba lomaliza la kabukuka kuti mukope chidwi cha munthuyo, komanso mumusonyeze mmene phunziro la Baibulo limachitikira. Anthu enanso osafunika kuwaiwala ndi amene anasonyezapo chidwi m’mbuyomu komanso maulendo obwereza. Ngakhale kuti panthawiyo anakana kuphunzira, panopa akhoza kuchita chidwi ndi kabukuka komanso njira yatsopano imene tikugwiritsa ntchito pophunzira. Musasiye kabukuka pakhomo pamene palibe anthu, kapena kutumiza limodzi ndi makalata kwa anthu amene sanasonyeze chidwi m’mbuyomu. Komiti ya Utumiki ya Mpingo ingakonze misonkhano yowonjezera yokonzekera utumiki m’mwezi umenewu.

  • Njira Zina: Ngati mpingo wanu umagwiritsa ntchito timashelefu, muikepo timabuku takuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Afotokozereni anthu amene asonyeza chidwi kuti tikhozanso kumaphunzira nawo Baibulo pogwiritsa ntchito kabukuka. Tingawasonyeze mwachidule mmene phunziro la Baibulo limachitikira, kapena tingapangane nawo kuti tidzawasonyeze nthawi ina. Woyang’anira utumiki angakonze zoti ofalitsa oyenerera akalalikire ku dera la malonda limene lili m’gawo lawo. Mungayambitsenso maphunziro a Baibulo kwa anthu amene mumagwira nawo ntchito kapena amene mumakumana nawo mukamalalikira mwamwayi.

Yesu anatilamula kuti ‘tiphunzitse anthu.’ (Mt 28:19, 20) Tikukhulupirira kuti ntchito yapaderayi itithandiza kukwaniritsa cholinga chathuchi pogwiritsa ntchito kabuku kakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale.