MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Mumayesetsa Kuona Mmene Yehova Akuyankhira Mapemphero Anu?
M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za mapemphero amene Mulungu anayankha. Atumiki a Mulungu ataona mmene iye anayankhira mapemphero awo komanso mmene anawathandizira, chikhulupiriro chawo chinalimba kwambiri. Choncho nafenso tiyenera kumapereka mapemphero achindunji kenako n’kumaona mmene Yehova akutiyankhira. Koma tizikumbukira kuti nthawi zina akhoza kutiyankha zosiyana ndi zimene tinapempha kapenanso zoposa zimene tinapempha. (2Ak 12:7-9; Aef 3:20) Kodi Yehova angatiyankhe m’njira ziti?
-
Angatithandize kukhala ndi mphamvu, kukhazikitsa mtima m’malo kapena kukhala ndi chikhulupiriro cholimba kuti tithe kulimbana ndi mavuto.—Afi 4:13
-
Angatipatse nzeru kuti tizisankha zinthu moyenera.—Yak 1:5
-
Angatithandize kuchita zimene iye amakonda.—Afi 2:13
-
Angatithandize kudekha tikapanikizika ndi nkhawa.—Afi 4:6, 7
-
Angatithandize pogwiritsa ntchito anthu ena.—1Yo 3:17, 18
ONERANI VIDIYO YAKUTI YEHOVA NDI “WAKUMVA PEMPHERO,” KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi zimene M’bale Shimizu anakumana nazo zingatilimbikitse bwanji ngati tikulephera kuchita zinthu zina chifukwa cha mavuto a thanzi?
-
Kodi tingatsanzire bwanji chitsanzo cha M’bale Shimizu?