CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kodi Mumapereka Nsembe?
Davide anauzidwa kuti amange guwa la nsembe pamalo opunthira mbewu a Arauna (2Sa 24:18)
Arauna ananena kuti apereka malo komanso nyama zoti apereke nsembe (2Sa 24:21-23)
Davide sakanapereka nsembe popanda kulipira (2Sa 24:24, 25; it-1 146)
Yehova amasangalala tikamapereka nthawi yathu, mphamvu zathu komanso zinthu zathu ndi mtima wonse kuti zinthu za Ufumu ziziyenda bwino. (w12 1/15 18 ¶8) Kodi mungakhale ndi zolinga zotani kuti muwonjezere ‘nsembe zimene mumapereka potamanda’ Mulungu?—Ahe 13:15.