Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ezara akuwerengera anthu Chilamulo komanso akutamanda Yehova

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Chimwemwe Chimene Yehova Amapereka Ndicho Malo Anu Achitetezo”

“Chimwemwe Chimene Yehova Amapereka Ndicho Malo Anu Achitetezo”

Anthu anasonkhana kuti amvetsere pamene Ezara ankawerenga Chilamulo (Ne 8:1, 2; w13 10/15 21 ¶2; onani chithunzi chapachikuto)

Iyi inali nthawi yoti anthuwo asangalale ndi kulambira Yehova, osati yoti azilira chifukwa cha machimo omwe anachita m’mbuyo (Ne 8:9, 11, 12)

Chimwemwe chimene Yehova amapereka ndi malo achitetezo kwa atumiki ake (Ne 8:10; w07 7/15 22 ¶9-10)

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndili ndi zifukwa ziti zimene zingandipangitse kukhala wosangalala, ngakhale kuti ndikukumana ndi mavuto?’