MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Zochita Zanu Zingathandize Banja Lanu Kukhala Losangalala
Yehova amafuna kuti mabanja azikhala osangalala. (Sl 127:3-5; Mla 9:9; 11:9) Komabe, chimwemwe chathu chikhoza kusokonezedwa chifukwa cha zochitika za m’dzikoli kapena zolakwitsa za anthu a m’banja lathu. Kodi aliyense m’banja angatani kuti athandize kuti banjalo likhale losangalala?
Mwamuna amapereka ulemu kwa mkazi wake. (1Pe 3:7) Amapeza nthawi yocheza naye. Sayembekezera zambiri zoposa zimene mkazi wake angakwanitse ndiponso amasonyeza kuti amayamikira chifukwa cha zimene amamuchitira komanso zimene amachitira banja lake. (Akl 3:15) Amamusonyeza chikondi komanso amamutamanda.—Miy 31:28, 31.
Mkazi amapeza njira zimene angathandizire mwamuna wake. (Miy 31:12) Amamugonjera komanso amachita naye zinthu mogwirizana. (Akl 3:18) Amalankhula naye mokoma mtima ndiponso amalankhula zabwino zokhudza mwamunayo.—Miy 31:26.
Makolo amapeza nthawi yocheza ndi ana awo. (De 6:6, 7) Amawauza ana awo kuti amawakonda. (Mt 3:17) Akamawalangiza, amachita nawo zinthu mwachikondi komanso mozindikira.—Aef 6:4.
Ana amalemekeza komanso amamvera makolo awo. (Miy 23:22) Amawafotokozera zimene akuganiza komanso mmene akumvera. Amamvera malangizo ochokera kwa makolo awo ndipo amawapatsa ulemu.—Miy 19:20.
ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZISANGALALA M’BANJA MWANU, KENAKO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:
Kodi aliyense anachita zotani kuti athandize banjali kukhala losangalala?