August 21-27
NEHEMIYA 10-11
Nyimbo Na. 37 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Anasiya Zinthu Zina Chifukwa cha Yehova”: (10 min.)
Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Ne 10:34—N’chifukwa chiyani anthu ankafunika kupititsa nkhuni ku nyumba ya Mulungu? (w06 2/1 11 ¶1)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (4 min.) Ne 10:28-39 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (3 min.) Yambani ndi nkhani imene ili mu chitsanzo cha ulendo woyamba. Muitanireni ku misonkhano yathu ndipo yerekezerani kumuonetsa vidiyo yakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? (th phunziro 1)
Ulendo Wobwereza: (4 min.) Yambani ndi nkhani imene ili mu chitsanzo cha ulendo wobwereza. Kenako mugawireni kabuku kakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, ndipo kambiranani naye mwachidule kamutu kakuti “Zimene Mungachite Kuti Muzipindula ndi Phunziro Lililonse.” (th phunziro 4)
Nkhani: (5 min.) w11 2/15 15-16 ¶12-15—Mutu: Nsembe Zimene Mulungu Amavomereza Masiku Ano. (th phunziro 20)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Kodi Muli ndi Zolinga Zotani M’chaka Chautumiki Chikubwerachi?”: (10 min.) Nkhani yokambirana.
“Ntchito Yapadera Yolengeza za Ufumu wa Mulungu mu September”: (5 min.) Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Limbikitsani anthu kuti adzagwire ntchitoyi mwakhama, ndipo fotokozani zimene mpingo wanu wakonza.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) lff phunziro 55 mfundo 1-4
Mawu Omaliza (3 min.)
Nyimbo Na. 92 ndi Pemphero