Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Muli ndi Zolinga Zotani M’chaka Chautumiki Chikubwerachi?

Kodi Muli ndi Zolinga Zotani M’chaka Chautumiki Chikubwerachi?

Zolinga zauzimu zimaphatikizapo chilichonse chimene timayesetsa kuchita kuti tizitumikira Yehova mokwanira komanso tizimusangalatsa. Kukhala ndi zolinga komanso kuzikwaniritsa kumatithandiza kukhala Akhristu olimba mwauzimu ndipo ndi njira yabwino kwambiri imene tingagwiritsire ntchito nthawi ndi mphamvu zathu. (1Ti 4:15) N’chifukwa chiyani tiyenera kumafufuza zolinga zathu nthawi zonse? Chifukwa zochitika pa moyo zimasintha. Cholinga chimene munali nacho poyamba, mwina panopa sichingathekeso kuchikwaniritsa, kapena mwina munachikwaniritsa ndipo mukhoza kuwonjezera china.

Nthawi yabwino yoti mufufuze zolinga zanu ndi pamene chaka chautumiki chatsopano chatsala pang’ono kuyamba. Kodi mungakambirane nkhaniyi pa kulambira kwa pabanja ndi kusankha zolinga zimene mungazikwaniritse panokha kapena limodzi monga banja?

Kodi muli ndi zolinga zotani mu mbali zotsatirazi, nanga mwakonza zotani kuti muzikwaniritse?

Kuwerenga Baibulo, kuphunzira Baibulo panokha, kupezeka pa misonkhano, kuyankha.—w02 6/15 15 ¶14-15

Kulalikira.​—w23.05 27 ¶4-5

Makhalidwe a Chikhristu.​—w22.04 23 ¶5-6

Zina: