Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Ntchito Yapadera Yolengeza za Ufumu wa Mulungu mu September

Ntchito Yapadera Yolengeza za Ufumu wa Mulungu mu September

M’mwezi wa September, tidzagwira ntchito yapadera yothandiza anthu kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndi umene uthetse mavuto amene tikukumana nawo. (Mt 24:14) Kodi tidzagwira bwanji ntchitoyi? Tidzawerengere anthu ambiri lemba lililonse lomwe limanena za Ufumu wa Mulungu m’mweziwu. Ngati wina wasonyeza chidwi, mudzam’patse magazini yogawira ya Nsanja ya Olonda Na. 2 2020. Kenako tidzabwerere mwachangu kwa anthu amene asonyeza chidwi ndipo tidzayambe kuphunzira nawo Baibulo pogwiritsa ntchito kabuku ka Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Amene adzachite upainiya wothandiza m’mwezi wa September, adzasankha kuchita wa maola 15 kapena 30.

Posachedwapa, Ufumu wa Mulungu uphwanya maulamuliro onse amene amatsutsa Ufumuwu. (Da 2:44; 1Ak 15:24, 25) Tiyeni tidzayesetse kugwira nawo ntchito yapaderayi kuti tidzasonyeze kuti tili ku mbali ya Yehova komanso Ufumu wake.