Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Muzikhala Okhulupirika kwa Yehova Mukamasankha Anthu Ocheza Nawo

Muzikhala Okhulupirika kwa Yehova Mukamasankha Anthu Ocheza Nawo

Aamoni komanso Amowabu sankaloledwa ‘kulowa mumpingo’ chifukwa anali ndi mbiri yoti ankatsutsa anthu a Mulungu (Ne 13:1, 2; it-1 95 ¶5)

Mkulu wa Ansembe Eliyasibu analola munthu wa Chiamoni kuti azigwiritsa ntchito chipinda chodyera cha m’kachisi (Ne 13:4, 5; w13 8/15 4 ¶5-6)

Nehemiya anasonyeza kuti anali wokhulupirika kwa Yehova mwa kuthetsa mgwirizano umene unalipo pakati pa Eliyasibu ndi mdani wa Mulungu (Ne 13:7-9)

Kodi tingakhale okhulupirika kwa Yehova ngati timacheza ndi anthu amene samutumikira?​—w96 3/15 16 ¶6.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi Yehova amamva bwanji akaona anthu amene ndimasankha kucheza nawo?’