Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tsanzirani Chikondi Chokhulupirika cha Yehova

Tsanzirani Chikondi Chokhulupirika cha Yehova

Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yosonyeza chikondi chokhulupirika. (Sl 103:11) Chikondi chimenechi sikuti chimangokhalapo kwa kanthawi kochepa kenako n’kutha. Chikondi chokhulupirika chimakhala champhamvu komanso chimakhalitsa. Yehova anasonyeza khalidwe limeneli kwa anthu ake Aisiraeli m’njira zambiri. Iye anawamasula ku ukapolo ku Iguputo ndipo analowetsa m’Dziko Lolonjezedwa. (Sl 105:42-44) Ankawamenyera nkhondo komanso ankawakhululukira mobwerezabwereza akachimwa. (Sl 107:19, 20) Kuchita “chidwi ndi ntchito za Yehova zosonyeza kukoma mtima kwake kosatha, [chikondi chokhulupirika]” kumatilimbikitsa kuti tizimutsanzira.​—Sl 107:43.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZICHITA CHIDWI NDI NTCHITO ZA YEHOVA ZOSONYEZA CHIKONDI CHOKHULUPIRIKA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi tingasonyeze chikondi chokhulupirika m’njira ziti?

  • N’chifukwa chiyani kusonyeza chikondi chokhulupirika kumafuna kusiya zinthu zina?