MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Amachita Khama Kuti Atitumikire
Oyang’anira madera ndi akazi awo amasonyeza chikondi chololera kuvutikira anthu amene amawatumikira. Mofanana ndi ena tonse, nawonso amafunikira zinthu zina, nthawi zina amatopa, amafooka komanso amakhala ndi nkhawa. (Yak 5:17) Komabe, mlungu uliwonse iwo amaganizira mmene angalimbikitsire abale ndi alongo a mumpingo umene akuchezera. Kunena zoona, oyang’anira dera amafunika “apatsidwe ulemu waukulu.”—1Ti 5:17.
Pamene mtumwi Paulo ankakonzekera kupita ku Roma kuti ‘akagawire abale a mpingo wa kumeneko mphatso inayake yauzimu,’ ankayembekezera mwachidwi kuti akalimbikitsane nawo mwa ‘chikhulupiriro chake ndi chawo.’ (Aro 1:11, 12) Kodi munaganizirapo za mmene mungalimbikitsire woyang’anira dera ndi mkazi wake, ngati ali wokwatira?
ONERANI VIDIYO YAKUTI MOYO WA WOYANG’ANIRA DERA AMENE AMATUMIKIRA MADERA A KU MIDZI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi oyang’anira madera ndi akazi awo amasonyeza chikondi chololera kuvutikira ena m’njira ziti?
-
Kodi zomwe amachita zakuthandizani bwanji?
-
Kodi tingawalimbikitse bwanji?