Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kokkinakis v. Greece: Droit réservé

Kuyambira kumanzere m’mwamba: West Virginia State Board of Education v. Barnette; Kokkinakis v. Greece; Taganrog LRO and Others v. Russia; Cha and Others v. South Korea

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

“Kuteteza . . . ndi Kukhazikitsa Mwalamulo Ntchito ya Uthenga Wabwino”

“Kuteteza . . . ndi Kukhazikitsa Mwalamulo Ntchito ya Uthenga Wabwino”

Pamene otsutsa anafuna kuletsa ntchito yomanganso kachisi imene Aisiraeli ankagwira, Aisiraeliwo anachita zomwe akanatha kuti mwalamulo, akhale ndi ufulu wopitiriza kugwira ntchito yawo. (Eza 5:11-16) Mofanana ndi zimenezi, Akhristu masiku ano amayesetsa kuteteza ndi kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya uthenga wabwino. (Afi 1:7) Kuti zimenezi zitheke, panakhazikitsidwa Dipatimenti ya Zamalamulo ku likulu la padziko lonse mu 1936. Masiku ano, dipatimentiyi imakonza zoti ntchito ya Ufumu izikhala yotetezeka padziko lonse. Kodi dipatimenti imeneyi yathandiza bwanji kuti ntchito ya Ufumu iziyenda bwino, nanga yathandiza bwanji abale ndi alongo?

ONERANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE ZIMACHITIKA MU DIPATIMENTI YA ZAMALAMULO KU LIKULU LAPADZIKO LONSE, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi a Mboni za Yehova akumana ndi mavuto ati okhudza nkhani zamalamulo?

  • Kodi ndi milandu iti imene a Mboni za Yehova awina? Perekani chitsanzo

  • Kodi tingachitepo chiyani poteteza ndi “kukhazikitsa mwalamulo ntchito ya uthenga wabwino”?

  • Kodi tingapeze pati pa webusaiti yathu nkhani zokhudza malamulo zomwe zimakhudza anthu a Mulungu komanso mayina a a Mboni za Yehova omwe akanali m’ndende chifukwa cha zimene amakhulupilira?