CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Musakalowerere Ntchito Yomanga”
Mkulu wa Ansembe Yesuwa (Yoswa) komanso Bwanamkubwa Zerubabele, anatsogolera pa ntchito yomanganso kachisi ngakhale kuti ntchitoyo inaletsedwa (Eza 5:1, 2; w22.03 18 ¶13)
Pamene otsutsa anafunsa kuti ndi ndani amene anawaloleza kugwira ntchitoyo, Ayuda anatchula za lamulo limene Koresi anapereka (Eza 5:3, 17; w86 2/1 29, bokosi ¶2-3)
Mfumu inatsimikizira kuti inaperekadi lamulolo ndipo inalamula otsutsawo kuti asalowerere pa ntchitoyo (Eza 6:7, 8; w22.03 15 ¶7)
FUNSO LOFUNIKA KULIGANIZIRA: Kodi nkhani ya m’Baibuloyi ikutithandiza bwanji kutsatira malangizo ochokera kwa anthu omwe Yehova anawasankha kuti azititsogolera ngakhale kuti sitikumvetsa malangizowo?—w22.03 18 ¶16.