Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

August 19-25

MASALIMO 75-77

August 19-25

Nyimbo Na. 120 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. N’chifukwa Chiyani Sitiyenera Kudzitukumula?

(10 min.)

Mulungu sasangalala ndi anthu odzitukumula (Sl 75:4; 1Ti 3:6; w18.01 28 ¶4-5)

Maudindo kapena mautumiki alionse amene timawalandira mumpingo ndi mphatso yochokera kwa Yehova ndipo sasonyeza kuti ndife anthu apadera (Sl 75:5-7; w06 7/15 11 ¶3)

Anthu onyada ngati atsogoleri adzikoli, Mulungu adzawachititsa manyazi (Sl 76:12)

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 76:10—Kodi “mkwiyo wa munthu” ungachititse bwanji kuti Yehova atamandidwe? (w06 7/15 11 ¶4)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Gwiritsani ntchito vidiyo yopezeka pa jw.org m’chilankhulo chomwe munthuyo amakonda. (lmd phunziro 1 mfundo 4)

5. Ulendo Woyamba

(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Mukhale okonzeka kusintha ngati munthuyo wakuuzani kuti sakhulupirira kuti kuli Mulungu. (lmd phunziro 2 mfundo 5)

6. Kuphunzitsa Anthu

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 127

7. Muzikhala Okhulupirika Anthu Akamakuyamikirani

(7 min.) Nkhani yokambirana.

Onerani VIDIYO yakuti Muzikhala Okhulupirika Ngati Mmene Yesu Analili—Mukamatamandidwa. Kenako funsani funso ili:

  • Kodi mwaphunzira chiyani kuchokera pa mmene Sergei anayankhira modzichepetsa pamene anthu ankamutamanda?

8. Ntchito Yapadera Yoyambitsa Maphunziro a Baibulo Pogwiritsa Ntchito Kabuku kapena Buku la Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale

(8 min.) Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Limbikitsani omvera kuti adzagwire nawo ntchitoyi mwakhama ndipo fotokozani zimene mpingo wanu wakonza.

9. Phunziro la Baibulo la Mpingo

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 95 ndi Pemphero