Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

August 26–September 1

SALIMO 78

August 26–September 1

Nyimbo Na. 97 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Kusakhulupirika kwa Aisiraeli Ndi Chitsanzo Chotichenjeza

(10 min.)

Aisiraeli anaiwala ntchito zodabwitsa za Yehova (Sl 78:11, 42; w96 12/1 29-30)

Aisiraeli sanayamikire zimene Yehova anawachitira (Sl 78:19; w06 7/15 17 ¶16)

Aisiraeli sanaphunzirepo kanthu pa zimene analakwitsa, m’malomwake anapitirizabe kukhala osakhulupirika (Sl 78:40, 41, 56, 57; w11 7/1 10 ¶3-4)


FUNSO LOFUNIKA KULIGANIZIRA: Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova?

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 78:24, 25—N’chifukwa chiyani mana amatchedwa “tirigu wochokera kumwamba” ndiponso “chakudya cha amphamvu”? (w06 7/15 11 ¶5)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pemphani mwininyumba kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 5 mfundo 5)

5. Ulendo Woyamba

(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Gwiritsani ntchito kapepala kuti muyambe kukambirana. (lmd phunziro 5 mfundo 4)

6. Ulendo Woyamba

(1 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Mwininyumba wakuuzani kuti ali ndi nthawi yochepa. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 2 mfundo 5)

7. Ulendo Woyamba

(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Popanda kutchula zokhudza Baibulo, chezani ndi munthuyo m’njira yoti adziwe kuti ndinu wa Mboni za Yehova, ndipo m’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 2 mfundo 4)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 96

8. Zimene Tingaphunzire Kuchokera kwa Mlaliki Filipo

(15 min.) Nkhani yokambirana.

M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu abwino komanso oipa. Kuti zitsanzozi zitithandize, timafunika kupeza nthawi yoti tiziphunzire. Kuwonjezera pa kuwerenga nkhanizi, tiziganizira mozama zomwe tikuphunzirapo, n’kusintha zochita zathu.

Mlaliki Filipo anali Mkhristu amene ankadziwika bwino kuti “ali ndi mzimu komanso nzeru.” (Mac 6:3, 5) Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo chake?

Onerani VIDIYO yakuti Zimene Tingaphunzire kwa Filipo. Kenako funsani omvera zimene aphunzira pa:

  • Zimene Filipo anachita zinthu zitasintha mwadzidzidzi.—Mac 8:1, 4, 5

  • Madalitso amene Filipo anapeza chifukwa chodzipereka kupita kumene kunkafunikira olalikira Ufumu ambiri.—Mac 8:6-8, 26-31, 34-40

  • Mmene kukhala ochereza kunathandizira Filipo ndi anthu a m’banja lake.—Mac 21:8-10

  • Mmene banja la muvidiyoyi linasangalalira chifukwa chotengera chitsanzo cha Filipo

9. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 14 ¶11-20

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 101 ndi Pemphero