Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

August 5-11

MASALIMO 70-72

August 5-11

Nyimbo Na. 59 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. ‘Uzani M’badwo Wotsatira’ za Mphamvu za Mulungu

(10 min.)

Davide ali mnyamata anaona Yehova akumuteteza (Sl 71:5; w99 9/1 18 ¶17)

Davide anaona kuti Yehova ankamuthandiza pamene anakalamba (Sl 71:9; g04 10/8 17 ¶3)

Davide analimbikitsa achinyamata powafotokozera zimene zinamuchitikira (Sl 71:17, 18; w14 1/15 23 ¶4-5)

DZIFUNSENI KUTI, ‘Pa nthawi ya kulambira kwa pabanja, kodi ndingacheze ndi m’bale kapena mlongo uti mu mpingo wathu amene watumikira Yehova kwa nthawi yaitali?’

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 72:8—Kodi zimene Yehova analonjeza Abulahamu pa Genesis 15:18 zinakwaniritsidwa bwanji pa nthawi imene Mfumu Solomo inkalamulira? (it-1 768)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Siyani mwamtendere kukambirana ndi munthu amene wayamba kukangana nanu. (lmd phunziro 4 mfundo 5)

5. Ulendo Wobwereza

(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Pitirizani kukambirana ndi wachibale amene amazengereza kuphunzira Baibulo. (lmd phunziro 8 mfundo 4)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

(5 min.) Nkhani. ijwfq 49​—Mutu: N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Anasintha Zinthu Zina Zomwe Ankakhulupirira? (th phunziro 17)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 76

7. Zomwe Mungachite pa Kulambira kwa Pabanja

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Nthawi ya Kulambira kwa Pabanja ndi yofunika kwambiri kuti ana ‘apatsidwe malangizo komanso aphunzitsidwe mogwirizana ndi zimene Yehova amanena.’ (Aef 6:4) Kuphunzitsa ana ndi ntchito yaikulu, koma kukhoza kukhala kosangalatsa makamaka ngati ana akufuna kudziwa zambiri zokhudza choonadi cha m’Baibulo. (Yoh 6:27; 1Pe 2:2) Kambiranani bokosi lakuti “ Zimene Mungakambirane pa Kulambira kwa Pabanja,” lomwe lili ndi mfundo zomwe zingathandize makolo kudziwa zimene angachite kuti Kulambira kwa Pabanja kuzikhala kothandiza komanso kosangalatsa, kenako kambiranani mafunso otsatirawa:

  • Kodi mungakonde kugwiritsa ntchito zinthu ziti?

  • Kodi pali zinanso zimene mwaona kuti ndi zothandiza?

Onerani VIDIYO yakuti Muzipeza Njira Zatsopano Zochitira Kulambira kwa Pabanja. Kenako funsani funso ili:

  • Kodi mwamuna angatani kuti mkazi wake azisangalala ndi kulambira kwa pabanja ngati pakhomopo palibe ana?

8. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 13 ¶17-24

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 123 ndi Pemphero