Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

July 15-21

MASALIMO 63-65

July 15-21

Nyimbo Na. 108 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. “Chikondi Chanu Chokhulupirika N’chabwino Kuposa Moyo”

(10 min.)

Kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu n’kofunika kwambiri kuposa kukhala ndi moyo (Sl 63:3; w01 10/15 15-16 ¶17-18)

Kuganizira mozama mmene Yehova amasonyezera chikondi chokhulupirika kumatichititsa kuti tizimukonda kwambiri (Sl 63:6; w19.12 28 ¶4; w15 10/15 24 ¶7)

Kuyamikira chikondi chokhulupirika cha Yehova kumatichititsa kuti tizimutamanda mosangalala (Sl 63:4, 5; w09 7/15 16 ¶6)

ZOMWE MUNGACHITE PA KULAMBIRA KWA PABANJA: Kambiranani mmene Yehova wakusonyezerani chikondi chokhulupirika.

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 64:3—Kodi vesili likutilimbikitsa bwanji kuti tizilankhula bwino? (w07 11/15 15 ¶6)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(2 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Mwininyumba salankhula chilankhulo chanu. (lmd phunziro 3 mfundo 4)

5. Ulendo Woyamba

(2 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Mwasiya kulankhula ndi munthu musanamulalikire. (lmd phunziro 2 mfundo 4)

6. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Pezani nkhani yomwe ingasangalatse munthuyo ndipo konzani zoti mudzakumanenso. (lmd phunziro 1 mfundo 5)

7. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

(4 min.) Chitsanzo. ijwfq 51​—Mutu: N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Amabwereranso Kunyumba za Anthu Omwe Anakana Kuti Awalalikire? (lmd phunziro 4 mfundo 3)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo 154

8. Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Timakonda Mulungu?

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Yehova ndi “wachikondi chokhulupirika chochuluka.” (Sl 86:15) Munthu amene ali ndi ‘chikondi chokhulupirika’ amakonda kwambiri munthu wina n’kupitirizabe kukhala wokhulupirika kwa iye zivute zitani. Ngakhale kuti Yehova amasonyeza chikondi kwa anthu onse, iye amasonyeza ‘chikondi chokhulupirika’ makamaka kwa atumiki ake omwe amakhala nawo pa ubwenzi wapadera. (Sl 33:18; 63:3; Yoh 3:16; Mac 14:17) Nafenso tingasonyeze kuti timayamikira chikondi chokhulupirika cha Yehova tikamamukonda. Tingachite zimenezi tikamamvera malamulo ake, kuphatikizapo lakuti “mukaphunzitse anthu.”—Mt 28:19; 1Yo 5:3.

Onerani VIDIYO yakuti Muzisonyeza Chikondi Chosatha mu Utumiki. Kenako funsani mafunso awa:

Kodi chikondi chingatilimbikitse bwanji kulalikira uthenga wabwino pamene

  • tatopa?

  • tikutsutsidwa?

  • tikuchita zinthu zathu za tsiku ndi tsiku?

9. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 12 ¶14-20

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 79 ndi Pemphero