July 22-28
MASALIMO 66-68
Nyimbo Na. 7 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Yehova Amanyamula Katundu Wathu Tsiku Lililonse
(10 min.)
Yehova amamvetsera tikamapemphera ndipo amatiyankha (Sl 66:19; w23.05 12 ¶15)
Yehova amadziwa bwino zimene anthu amene akukumana ndi mavuto amafunikira (Sl 68:5; w10 12/1 23 ¶6; w09 4/1 31 ¶1)
Yehova amatithandiza tsiku lililonse (Sl 68:19; w23.01 19 ¶17)
FUNSO LOFUNIKA KULIGANIZIRA: Kodi timalola bwanji Yehova kuti atinyamulire katundu wathu?
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
-
Sl 68:18—M’nthawi ya Aisiraeli akale, kodi ‘anatenga amuna ati kuti akhale mphatso’? (w06 6/1 10 ¶5)
-
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Sl 66:1-20 (th phunziro 11)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Mwininyumba ndi wa chikhalidwe chosiyana ndi chanu. (lmd phunziro 5 mfundo 3)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pitirizani kukambirana za kapepala komwe munamusiyira pa ulendo wapita. (lmd phunziro 9 mfundo 3)
6. Kuphunzitsa Anthu
Nyimbo Na. 102
7. Kodi Munganyamuleko Katundu wa Munthu Wina?
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Palibe mtumiki wa Mulungu aliyense amene angalimbane ndi mavuto payekha. (2Mb 20:15; Sl 127:1) Yehova ndi amene amatithandiza. (Yes 41:10) Kodi Yehova amatithandiza bwanji? Amatipatsa malangizo kudzera m’Mawu ake komanso m’gulu lake. (Yes 48:17) Amatipatsa mzimu wake woyera womwe ndi wamphamvu. (Lu 11:13) Komanso amachititsa abale ndi alongo athu kuti atilimbikitse komanso atithandize. (2Ak 7:6) Zimenezi zikutanthauza kuti Yehova akhoza kugwiritsa ntchito aliyense wa ife kuti anyamuleko katundu wa Mkhristu mnzake.
Onerani VIDIYO yakuti Muzisonyeza Chikondi Chosatha Mumpingo Wachikhristu—Muzikonda Achikulire. Kenako funsani omvera funso ili:
-
Kodi mungachite zinthu ziti kuti munyamuleko katundu wa Mkhristu wachikulire?
Onerani VIDIYO yakuti Muzisonyeza Chikondi Chosatha Mumpingo Wachikhristu—Muzikonda Amene Akuchita Utumiki wa Nthawi Zonse. Kenako funsani omvera funso ili:
-
Kodi mungachite zinthu ziti kuti munyamuleko katundu wa amene akuchita utumiki wa nthawi zonse?
Onerani VIDIYO yakuti Muzisonyeza Chikondi Chosatha Mumpingo Wachikhristu—Muzikonda Anthu Ochokera Kumayiko Ena. Kenako funsani omvera funso ili:
-
Kodi mungachite zinthu ziti kuti munyamuleko katundu wa amene akukumana ndi mayesero aakulu?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 13 ¶1-7, mawu ofotokoza gawo 5 ndi bokosi patsamba 103