MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Mulungu Ndiye Mthandizi Wanga”
Masalimo 52–59 amasonyeza mmene Davide ankamvera pa nthawi yomwe ankakumana ndi mavuto. Komabe anakhulupirira Yehova pa nthawi yovutayi. (Sal. 54:4; 55:22) Iye anatamandanso Yehova chifukwa cha Mawu ake. (Sal. 56:10) Kodi ifeyo timakhulupirira komanso kudalira Mulungu ngati mmene Davide ankachitira? Kodi tikakumana ndi mavuto, timafufuza malangizo m’Mawu a Yehova? (Miy. 2:6) Kodi ndi mavesi ati omwe anakuthandizani pamene . . .
-
munafooka kapena kuvutika maganizo?
-
munkadwala?
-
ena anakukhumudwitsani?
-
munkazunzidwa?