June 6-12
MASALIMO 34-37
Nyimbo Na. 95 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Khulupirira Yehova Ndipo Chita Zabwino”: (10 min.)
Sal. 37:1, 2—Pitirizani kutumikira Yehova osati kusirira anthu ochita zosalungama omwe akuoneka ngati zinthu zikuwayendera bwino (w03 12/1 9-10 ndime 3-6)
Sal. 37:3-6—Muzikhulupilira Yehova, muzichita zabwino ndipo iye adzakudalitsani (w03 12/1 10-12 ndime 7-15)
Sal. 37:7-11—Muziyembekezera Yehova moleza mtima kuti adzachotse anthu oipa (w03 12/1 13 ndime 16-20)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Sal. 34:18—Kodi Yehova amayankha bwanji mapemphero a “anthu a mtima wosweka” ndiponso “odzimvera chisoni mumtima mwawo”? (w11 6/1 19)
Sal. 34:20—Kodi ulosiwu unakwaniritsidwa bwanji pa Yesu? (w13 12/15 21 ndime 19)
Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Sal. 35:19–36:12
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kukonzekera Ulaliki wa Mwezi Uno: (15 min.) Nkhani yokambirana. Pambuyo poonetsa vidiyo ya chitsanzo cha ulaliki iliyonse payokha, kambiranani mfundo zikuluzikulu za m’vidiyoyo. Limbikitsani ofalitsa kuti alembe ulaliki wawowawo.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Nyimbo Na. 93
“Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Kugwiritsa Ntchito Mavidiyo Pophunzitsa”: (15 min.) Nkhani yokambirana. Kuti musonyeze mmene ofalitsa angagwiritsire ntchito mfundo zapakamutu kakuti, “Kodi Tingachite Bwanji Zimenezi?” onetsani vidiyo ya pa jw.org yakuti, Kodi Mlembi Wamkulu wa Baibulo Ndani? (Pitani pamene palembedwa kuti, MABUKU > MABUKU. Kenako pezani kabuku ka Uthenga Wabwino. Vidiyoyi mungaipeze pamutu wakuti: “Kodi Uthenga Wabwino ndi Wochokeradi kwa Mulungu?”)
Phunziro la Baibulo la Mpingo: cl mutu 31 ndime 13-20 (30 min.)
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 61 ndi Pemphero