MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzitsatira Mapazi a Khristu Mosamala Kwambiri
Yesu anatipatsa chitsanzo choti tizitsatira makamaka tikamakumana ndi mayesero kapena tikamazunzidwa. (1 Pet. 2:21-23) Iye sanabwezere anthu amene ankamunyoza ndipo sanachite zimenezi ngakhale pa nthawi imene ankamva ululu. (Maliko 15:29-32) Kodi n’chiyani chinamuthandiza kuti apirire? Iye anali wofunitsitsa kuchita chifuniro cha Yehova. (Yoh. 6:38) Yesu ankaganiziranso kwambiri za “chimwemwe chimene anamuikira patsogolo pake.”—Aheb. 12:2.
Kodi ifeyo timatani ngati anthu ena akutizunza chifukwa cha zimene timakhulupirira? Akhristu oona ‘sabwezera choipa pa choipa.’ (Aroma 12:14, 17) Tikamatsanzira Yesu n’kumapirira, tingakhalebe osangalala podziwa kuti Yehova akukondwera nafe.—Mat. 5:10-12; 1 Pet. 4:12-14.
ONERANI VIDIYO YAKUTI DZINA LA YEHOVA NDI LOFUNIKA KWAMBIRI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi Mlongo Pötzinger * anagwiritsa ntchito bwanji nthawi yake mwanzeru pamene anamutsekera m’selo yayekha?
-
Kodi M’bale ndi Mlongo Pötzinger anakumana ndi mavuto otani pamene anali m’ndende zosiyanasiyana?
-
Kodi n’chiyani chinawathandiza kuti apirire?
^ ndime 6 Dzinali limalembedwanso kuti Poetzinger.