MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzipindula Mokwanira Mukamaphunzira Panokha
KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Tikamaphunzira Mawu a Mulungu patokha, timadziwa bwino “m’lifupi ndi m’litali ndi kukwera ndi kuzama” kwa choonadi. (Aef. 3:18) Kuphunzira patokha kumatithandiza kuti tikhale osalakwa komanso opanda chilema m’dziko loipali. Kumatithandizanso kuti tipitirize “kugwira mwamphamvu mawu amoyo.” (Afil. 2:15, 16) Tikamaphunzira Mawu a Mulungu timatha kusankha zomwe tikufuna kuphunzira malinga ndi zimene tikufunikira. Kodi tingatani kuti tizipindula kwambiri tikamawerenga komanso kuphunzira Baibulo?
KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?
-
Muzilemba mzere kunsi kwa mavesi komanso notsi m’Baibulo lanu
-
Mukamawerenga Mawu a Mulungu muzidzifunsa mafunso monga akuti: ‘Nkhaniyi ikunena za ndani? Chinachitika n’chiyani? Zinachitikira kuti? Zinachitika bwanji? N’chifukwa chiyani zinachitika choncho?’
-
Muzifufuza. Mungagwiritse ntchito zipangizo zofufuzira zimene muli nazo ndipo mukhoza kufufuza pogwiritsa ntchito mitu ya nkhani kapena mavesi a m’Baibulo
-
Muziganizira mozama zimene mwawerengazo n’kuona mmene zikukukhudzirani
-
Muzigwiritsa ntchito zimene mwaphunzira.—Luka 6:47, 48
ONERANI VIDIYO YAKUTI PITIRIZANI “KUGWIRA MWAMPHAMVU MAWU AMOYO” POPHUNZIRA MWAKHAMA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi ena apindula bwanji chifukwa chophunzira pawokha?
-
N’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera tisanayambe kuphunzira patokha?
-
Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizimvetsa bwino zimene tikuwerenga m’Baibulo?
-
Kodi ndi zizindikiro ziti zomwe tingalembe m’Baibulo lathu tikamaphunzira patokha?
-
Kodi kuganizira zomwe tikuwerenga n’kofunika bwanji?
-
N’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsa ntchito zimene taphunzira?