MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Maganizo a Yehova Ndi Otani pa Nkhaniyi?
Tisanasankhe zochita pa nkhani iliyonse, kaya yaikulu kapena yaing’ono, tizidzifunsa kuti, ‘Kodi maganizo a Yehova ndi otani pa nkhaniyi?’ Ngakhale kuti sitingadziwe zonse zokhudza mmene Yehova amaganizira, Mawu ake angatithandize kuti tichite “ntchito iliyonse yabwino.” (2 Tim. 3:16, 17; Aroma 11:33, 34) Yesu ankadziwa bwino zimene Yehova amafuna ndipo ankachita zimenezo pa moyo wake. (Yoh. 4:34) Ifenso tiziyesetsa kutsanzira Yesu posankha zinthu zimene zingasangalatse Yehova.—Yoh. 8:28, 29; Aef. 5:15-17.
ONERANI VIDIYO YAKUTI PITIRIZANI KUZINDIKIRA CHIFUNIRO CHA YEHOVA (LEV. 19:18), KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
N’chifukwa chiyani tiyenera kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pa moyo wathu?
-
Kodi muyenera kuganizira mfundo za m’Baibulo ziti mukamasankha nyimbo?
-
Kodi muyenera kuganizira mfundo za m’Baibulo ziti pa nkhani ya zovala komanso kudzikongoletsa?
-
Kodi ndi pa nkhani zinanso ziti pomwe tingafunike kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo?
-
Kodi tingatani kuti tizidziwa bwino zimene Yehova amafuna kuti tizichita?