MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Mumasankha Zosangalatsa Mwanzeru?
N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osamala tikamasankha zosangalatsa? Chifukwa chake n’chakuti tikamasankha mafilimu, nyimbo, mawebusaiti, mabuku komanso masewera a pakompyuta, timakhala tikusankha zinthu zoti tilowetse m’maganizo athu. Zimene timasankha zimakhudza khalidwe lathu. N’zomvetsa chisoni kuti zosangalatsa zambiri masiku ano zimakhala ndi mbali zina zomwe Yehova amadana nazo. (Sal. 11:5; Agal. 5:19-21) N’chifukwa chake Baibulo limatilimbikitsa kuti tiziganizira zinthu zimene zingalemekeze Yehova.—Afil. 4:8.
ONERANI VIDIYO YAKUTI KODI NDIYENERA KUSANKHA ZOSANGALATSA ZOTANI? KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
-
Kodi masewera achiwawa omwe Aroma ankachita akufanana bwanji ndi zosangalatsa za masiku ano?
-
Kodi abale ndi alongo a mumpingo angathandize bwanji achinyamata kusankha bwino zosangalatsa?
-
Kodi lemba la Aroma 12:9 lingatithandize bwanji kuti tizisankha zosangalatsa mwanzeru?
-
Kodi ndi zosangalatsa zabwino ziti zomwe zimapezeka m’dera lanu?