Nkhani ‘Yophiphiritsira’ Yomwe ndi Yofunika Kwambiri kwa Ife
Mtumwi Paulo anafotokoza nkhani ‘yophiphiritsira’ pofuna kusonyeza kuti pangano latsopano ndi lofunika kwambiri kusiyana ndi pangano lachilamulo. Yesu komanso Akhristu odzozedwa adzathandiza anthu onse kuti amasuke ku uchimo, imfa komanso zopweteka.—Yes. 25:8, 9.
HAGARA, KAPOLO WAMKAZI Akuimira mtundu wa Isiraeli womwe unkatsatira Chilamulo ndipo likulu lawo linali ku Yerusalemu |
“ANA” A HAGARA Akuimira Ayuda (amene analonjeza kuti adzatsatira Chilamulo) omwe anakana komanso kuzunza Yesu |
AKAPOLO A PANGANO LACHILAMULO Chilamulo chinkakumbutsa Aisiraeli kuti anali akapolo a uchimo |
SARA, YEMWE ANALI MFULU Akuimira Yerusalemu wam’mwamba, yemwe ndi mbali yakumwamba ya gulu la Mulungu |
“ANA” A SARA Akuimira Khristu ndi Akhristu odzozedwa okwana 144,000 |
PANGANO LATSOPANO LIMAPEREKA UFULU Kukhulupirira nsembe ya Khristu kumabweretsa ufulu womwe umamasula munthu ku ukapolo wa Chilamulo |