MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Mmene Tingagwiritsire Ntchito Zitsanzo za Zimene Tinganene
Kuyambira mu January 2018, patsamba loyamba la Ndandanda ya Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu, pakhala pakuikidwa zitsanzo za zimene tinganene. Kodi tingazigwiritse ntchito bwanji?
Mukamakamba Nkhani za Ophunzira: Muzigwiritsa ntchito funso, lemba, komanso funso la ulendo wotsatira zomwe zili m’chitsanzo cha zimene tinganene. Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti muzinena ndendende zimene zili mu vidiyo ya zimene tinganene. Mukhoza kupanga chitsanzo chanu m’njira yosiyana ndi imene yagwiritsidwa ntchito m’vidiyo. Mungagwiritsenso ntchito mawu oyamba komanso kufotokoza mfundo za m’nkhani yanu mosiyana ndi zimene zili m’vidiyo. Mukhozanso kugawira buku kapena magazini opezeka mu Zinthu Zophunzitsira ngakhale kuti sizinatchulidwe m’malangizo a nkhani yanu.
Mukakhala mu Utumiki: Cholinga cha zitsanzo za zimene tinganene ndi kutithandiza kudziwa mfundo zina zomwe tikhoza kufotokoza mu utumiki. Ngati munthu atasonyeza kuti akufuna kudziwa zambiri, mukhoza kupitiriza kukambirana naye, mwina pogwiritsa ntchito mfundo za m’chitsanzo cha ulendo wobwereza. Mukhoza kusintha chitsanzocho kapena kugwiritsa ntchito chitsanzo china chosiyana ndi chimenecho. Kodi nkhani imene munkagwiritsa ntchito mwezi watha kapena lemba lina losiyana ndi limene mukugwiritsa ntchito panopa, zikhoza kukopa kwambiri chidwi cha anthu a m’dera lanu? Kodi anthu a m’dera limene mumakhala amachita chidwi ndi nkhani komanso zinthu zomwe zangochitika kumene m’deralo? Ngakhale kuti mukhoza kugwiritsa ntchito zitsanzo za zimene tinganene m’njira zosiyanasiyana, cholinga chanu chizikhala kuchita ‘zinthu zonse chifukwa cha uthenga wabwino, kuti muugawirenso kwa ena.’—1 Akor. 9:22, 23.