June 8-14
GENESIS 46-47
Nyimbo Na. 86 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Chakudya pa Nthawi ya Njala”: (10 min.)
Gen. 47:13—Ku Iguputo ndi ku Kanani kunagwa njala yaikulu (w87 5/1 15 ¶2)
Gen. 47:16, 19, 20—Aiguputo analolera kusiya zinthu zawo kuti akhale ndi moyo
Gen. 47:23-25—Pamafunika khama kuti tizipindula ndi chakudya chauzimu chomwe tili nacho (kr 234-235 ¶11-12)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Gen. 46:4—Kodi zimene Yakobo anauzidwa kuti Yosefe ndi amene ‘adzamutseke maso’ zinkatanthauza chiyani? (it-1 220 ¶1)
Gen. 46:26, 27—Kodi ndi anthu angati a m’banja la Yakobo omwe anakalowa m’dziko la Iguputo? (nwtsty mfundo zophunzirira, Mac. 7:14)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Gen. 47:1-17 (th phunziro 10)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi. Kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: Kodi wofalitsayu anagwiritsa ntchito bwanji mafunso mwaluso? Nanga anafotokoza bwanji lemba m’njira yomveka bwino?
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Kenako gawirani buku kapena magazini yopezeka pa Zinthu Zophunzitsira. (th phunziro 3)
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 5 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Kenako gawirani buku la Zimene Baibulo Limaphunzitsa ndipo yambitsani phunziro la Baibulo pogwiritsa ntchito mutu 9. (th phunziro 14)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzilola Kuti Yehova Azikukumbutsani: (15 min.) Onerani vidiyo yakuti Tiziyamikira Zikumbutso za Yehova. Limbikitsani onse kuti apitirize kuwerenga Mawu a Mulungu komanso kudya chakudya chonse chauzimu chomwe timalandira.—Yes. 25:6; 55:1; 65:13; Mat. 24:45.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 87
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 39 ndi Pemphero