Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Tidzalandire Bwino Alendo

Tidzalandire Bwino Alendo

Pamwambo wa Chikumbutso womwe udzachitike pa 23 March, tikuyembekezera kudzakhala ndi alendo oposa 12 miliyoni. Iwo adzakhala ndi mwayi womva za mphatso ya dipo limene Yehova anapereka komanso madalitso ena omwe tidzapeze chifukwa cha mphatso imeneyi. (Yes. 11:6-9; 35:5, 6; 65:21-23; Yoh. 3:16) Komabe alendowa adzaphunziranso zinthu zambiri kuchokera kwa ena tonsefe osati kwa wokamba nkhani yekha. Tonsefe tili ndi udindo wodzalandira bwino alendowa. (Aroma 15:7) Mwina tingadzachite zotsatirazi:

  • M’malo mongokhala pampando wathu n’kumadikira kuti mwambo uyambe, tingadzachite bwino kulandira mwansangala alendo komanso anthu amene anasiya kusonkhana

  • Posamalira anthu amene tinawaitana, tisadzaiwale anthu enanso amene ndi alendo pamwambowo. Tingadzawapemphe kuti tikhale nawo pamodzi n’kumaona limodzi Baibulo ndi nyimbo

  • Mwambowu ukadzatha, tidzapeze nthawi yoyankha mafunso awo. Ngati tikufunika kupereka mpata kuti mpingo wina uchitenso Chikumbutso, tingadzakonze zoti tikumane nawo pasanathe masiku ambiri. Alendo amene sitikudziwa kumene amakhala tingadzawafunse kuti: “Kodi ndingakupezeni bwanji kuti tidzakambirane mmene mwaonera mwambowu?”