Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zitsanzo za Ulaliki

Zitsanzo za Ulaliki

NSANJA YA OLONDA

Funso: Kodi mumadziwa zimene lemba ili limanena?

Lemba: Yoh. 3:16

Perekani Magaziniyo: Magaziniyi ikufotokoza mwayi umene tili nawo chifukwa choti Yesu analolera kuvutika mpaka kufa.

NSANJA YA OLONDA (tsamba lomaliza)

Funso: Taonani funso ili komanso zimene anthu ena amayankha. [Werengani funso loyamba ndi mayankho ake.] Kodi inuyo mungayankhe bwanji?

Lemba: Mat. 4:1-4

Perekani Magaziniyo: Zimenezi zikusonyeza kuti Mdyerekezi alikodi ndipo si mphamvu chabe ya zinthu zoipa, chifukwa ankayankhulana ndi Yesu n’kumamuyesa. Kodi ndi zinthu zinanso ziti zimene Baibulo limanena zokhudza Mdyerekezi? Werengani nkhaniyi kuti mumve zambiri.

KAPEPALA KOITANIRA ANTHU KU CHIKUMBUTSO

Perekani Kapepalako: Tikugawira anthu kapepala aka kowaitanira kumwambo wofunika kwambiri. [Apatseni kapepalako.] Pa 23 March, anthu ambiri padziko lonse adzasonkhana pamwambo wokumbukira imfa ya Yesu Khristu. Kudzakhala nkhani ya m’Baibulo yofotokoza mwayi umene tili nawo chifukwa cha imfa ya Yesu ndipo simudzafunikira kulipira kalikonse. Kapepalaka kakusonyeza nthawi ndi malo amene mwambowu udzachitikire kwathu kuno. Mudzayesetse kubwera.

LEMBANI ULALIKI WANUWANU

Potengera zitsanzozi, konzani njira imene mungagwiritse ntchito.