MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Tingagwiritse Ntchito Bwanji Kabuku Kakuti Mverani Mulungu?
Kabuku kakuti Mverani Mulungu kanapangidwa n’cholinga choti tizigwiritsa ntchito pophunzira ndi anthu amene amavutika kwambiri kuwerenga. Kamatithandiza kuphunzitsa mfundo zikuluzikulu za m’Baibulo pogwiritsa ntchito zithunzi. Phunziro lililonse ndi la masamba awiri ndipo lili ndi zithunzi zokonzedwa bwino zomwe zili ndi mivi yolozera chithunzi chotsatira.
Kabuku kakuti Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha kali ndi zithunzi zofanana ndi za m’kabuku kakuti Mverani Mulungu koma kali ndi mawu ambiriko ndipo tikhoza kukagwiritsa ntchito pophunzira ndi anthu amene savutika kwambiri kuwerenga. Ofalitsa ambiri amakonda kugwiritsa ntchito kabukuka akamaphunzira ndi anthu kabuku kakuti Mverani Mulungu. Masamba ambiri ali ndi kabokosi kamene kali ndi mfundo zowonjezera zomwe tingakambirane ndi wophunzira wathu ngati tikuona kuti angazimvetse.
Mukhoza kugawira timabukuti mwezi uliwonse. Mukamaphunzira timabukuti ndi anthu, muzigwiritsa ntchito zithunzi powafotokozera nkhani za m’Baibulo. Muzifunsa mafunso kuti wophunzira azinena maganizo ake komanso kuti mudziwe ngati akumvetsa zimene akuphunzirazo. Muziwerenga ndiponso kukambirana malemba amene ali m’munsi mwa tsamba lililonse. Mukamaliza kabukuka, mungayambe kuphunzira naye buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa kuti mumuthandize kudziwa zambiri ndiponso kubatizidwa.