Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Tingagwiritse Ntchito Bwanji Kabuku Kakuti Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?

Kodi Tingagwiritse Ntchito Bwanji Kabuku Kakuti Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?

Kabuku kakuti Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano? kanapangidwa n’cholinga choti tiziphunzira ndi munthu pa ulendo uliwonse tisanayambe kapena tikamaliza kuchita phunziro la Baibulo. * Mitu 1 mpaka 4 imathandiza anthu kuti atidziwe bwino, mitu 5 mpaka 14 imawathandiza kudziwa zimene timachita ndipo mitu 15 mpaka 28 imathandiza anthu kudziwa mmene gulu lathu limayendera. Zimakhala bwino kuphunzira kabukuka kuyambira mutu woyamba mpaka womaliza. Komabe mukhoza kukambirana mutu wina mwamsanga ngati mukuona kuti n’zofunika. Mitu ya m’kabukuka ndi yaifupi moti mukhoza kukambirana ndi munthu kwa maminitsi 5 kapena 10 okha basi.

  • Werengani funso lomwe ndi mutu wa nkhaniyo

  • Werengani limodzi mutu wonse kapena kuugawa m’zigawo

  • Kambiranani zimene mwawerengazo. Gwiritsani ntchito zithunzi komanso mafunso amene ali m’munsi mwa tsambalo. Werengani ndiponso kukambirana malemba amene mukuona kuti angathandize munthuyo. Mufotokozereni kuti mitu ing’onoing’ono imene ili ndi zilembo zakuda kwambiri imayankha funso la mutuwo

  • Ngati mutuwo uli ndi bokosi lakuti “Dziwani Zambiri,” liwerengeni n’kulimbikitsa munthuyo kuti atsatire malangizo ake

^ ndime 3 Kabuku kamene kali pa intaneti n’kamene kangokonzedwa kumene