Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 22-23

Muzitsatira Malamulo Awiri Aakulu Kwambiri

Muzitsatira Malamulo Awiri Aakulu Kwambiri

22:36-39

Pogwiritsa ntchito lemba la Mateyu 22:36-39, lembani manambala kuyambira ndi chifukwa chachikulu chimene timapitira kumisonkhano yathu:

  • Kuti tikalimbikitsidwe

  • Kuti tikalimbikitse ena

  • Kuti tikalambire komanso kusonyeza kuti timakonda Yehova

N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kupitabe kumisonkhano ngakhale titatopa kwambiri moti tikuona kuti sitingakapindule mokwanira?

Kodi ndi njira zina ziti zimene tingasonyezere kuti timamvera malamulo awiri aakulu kwambiri?