Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Azikonzekera

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Azikonzekera

KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Anthu amene tikuphunzira nawo Baibulo akamakonzekera, akhoza kumamvetsa komanso kukumbukira mfundo zimene tikuwaphunzitsa. Ndipo akamamvetsa komanso kukumbukira zimene aphunzira, akhoza kupita patsogolo mwamsanga. Ngakhale akabatizidwa, ayenera kupitiriza kukonzekera misonkhano komanso utumiki kuti ‘akhalebe maso.’ (Mat. 25:13) Choncho kuzolowera kuphunzira pawokha komanso kukonzekera nthawi zonse, kungadzawathandize kwa moyo wawo wonse. Ndiyetu ndi bwino kuti tikangoyamba kuphunzira ndi munthu, tizimuthandiza kuti azikonzekera phunzirolo.

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

  • Muziwasonyeza chitsanzo chabwino. (Aroma 2:21) Muzikonzekera nthawi iliyonse yomwe mukufuna kukachititsa phunziro ndipo muziganizira mmene mungathandizire wophunzirayo. (km 11/15 3) Muzimuonetsa buku lanu lodula mizere kunsi kwa mayankho

  • Muzimulimbikitsa kuti azikonzekera. Mukangoyamba kuphunzira ndi munthu, muzimuthandiza kudziwa kuti kukonzekera ndi mbali ya phunziro ndipo muzimuuza ubwino wake. Mungamuthandize kudziwa zomwe angamachite kuti azipeza nthawi yokonzekera. Ofalitsa ena amapereka buku lawo lodula mizere kunsi kwa mayankho kwa munthu amene akumuphunzitsa pofuna kumuthandiza kuona ubwino wokonzekera. Muzimuyamikira akakonzekera phunziro

  • Muzimusonyeza mmene angakonzekerere. Ofalitsa ena amasankha zoti phunziro likangoyamba kumene, amusonyeze munthu mmene angamakonzekerere pa nthawi yonse yomwe akuchita phunziro