Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 20-21

“Aliyense Wofuna Kukhala Wamkulu Pakati Panu Ayenera Kukhala Mtumiki Wanu”

“Aliyense Wofuna Kukhala Wamkulu Pakati Panu Ayenera Kukhala Mtumiki Wanu”

20:28

Alembi ndi Afarisi anali anthu onyada ndipo ankachita zinthu n’cholinga choti ena awaone komanso ankaima m’misika kuti anthu aziwapatsa moni

Alembi ndi Afarisi anali anthu onyada ndipo ankafuna kutchuka komanso kuti anthu aziwalemekeza. (Mat. 23:5-7) Koma Yesu sankachita zimenezo. Baibulo limati: “Mwana wa munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira.” (Mat. 20:28) Kodi timakonda kuchita utumiki umene ungachititse kuti ena aziona kuti ndife ofunika kwambiri komanso azitilemekeza? Ngati tikufuna kukhala wamkulu pamaso pa Yehova, tiyenera kuyesetsa kutengera chitsanzo cha Yesu n’kumagwira ntchito zothandiza ena. Nthawi zambiri ntchito ngati zimenezi sizichitikira pagulu ndipo ndi Yehova yekha amene amaona. (Mat. 6:1-4) Munthu wodzichepetsa . . .

  • amayeretsa komanso kukonza nawo Nyumba ya Ufumu

  • amathandiza achikulire komanso anthu ena

  • amapereka ndalama zake pothandiza ntchito zokhudza Ufumu