Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Tinganene

Zimene Tinganene

●○○ ULENDO WOYAMBA

Ntchito Yogawira Kapepala Koitanira Anthu ku Chikumbutso (March 3-31): Tikukuitanani ku mwambo wofunika kwambiri. Kapepala kanu ndi kameneka. Loweruka pa 31 March, anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse adzasonkhana kuti achite mwambo wokumbukira imfa ya Yesu Khristu. Kapepalaka kakusonyeza nthawi komanso malo omwe mwambowu udzachitikire m’dera lathu lino. Tikukuitananinso kuti mudzamvetsere nkhani ya mutu wakuti, “Kodi Yesu Khristu Ndi Ndani Kwenikweni?” yomwe idzakambidwe kutatsala mlungu umodzi kuti mwambowu uchitike.

Funso la Ulendo Wotsatira Ngati Wasonyeza Chidwi: N’chifukwa chiyani Yesu anafa?

○●○ ULENDO WOBWEREZA WOYAMBA

Funso: N’chifukwa chiyani Yesu anafa?

Lemba: Mat. 20:28

Funso la Ulendo Wotsatira: Kodi dipo la Yesu lingatithandize bwanji?

○○● ULENDO WOBWEREZA WACHIWIRI

Funso: Kodi dipo la Yesu lingatithandize bwanji?

Lemba: Aroma 6:23

Funso la Ulendo Wotsatira: Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira dipo?