March 18-24
1 AKORINTO 1-3
Nyimbo Na. 127 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Kodi Ndinu Munthu Wakuthupi Kapena Munthu Wauzimu?”: (10 min.)
[Onerani vidiyo yakuti Mfundo Zothandiza Kumvetsa Buku la 1 Akorinto.]
1 Akor. 2:14—Kodi kukhala “munthu wakuthupi” kumatanthauza chiyani? (w18.02 19 ¶4-5)
1 Akor. 2:15, 16—Kodi kukhala “munthu wauzimu” kumatanthauza chiyani? (w18.02 19 ¶6; 22 ¶15)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
1 Akor. 1:20—Kodi Mulungu amapangitsa bwanji “nzeru za dzikoli kukhala zopusa”? (it-2 1193 ¶1)
1 Akor. 2:3-5—Kodi chitsanzo cha Paulo chingatithandize bwanji? (w08 7/15 27 ¶6)
Kodi mwaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo zina ziti zothandiza zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) 1 Akor. 1:1-17 (th phunziro 10)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Woyamba: (5 min.) Onerani ndi kukambirana mfundo za m’vidiyoyi.
Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo wobwereza woyamba. (th phunziro 3)
Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 4 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza woyamba. Kenako musonyezeni buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa. (th phunziro 11)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzilemba Makalata Abwino”: (8 min.) Nkhani yokambirana.
Ntchito Yoitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba pa 23 March: (7 min.) Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Perekani kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso kwa aliyense n’kukambirana mfundo zake. Onerani ndi kukambirana vidiyo ya zimene tinganene pogawira kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso. Fotokozani zimene mpingo wanu wakonza kuti mudzathe kugawira timapepalati kwa anthu onse a m’gawo lanu.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 30
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 5 ndi Pemphero