Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kalata Yachitsanzo

Kalata Yachitsanzo
  • Muzigwiritsa ntchito adiresi yanu. Ngati mukuona kuti sizingakhale bwino kuigwiritsa ntchito, mukhoza kulemba adiresi ya Nyumba ya Ufumu ngati akulu atakulolani kuchita zimenezi. Koma simuyenera kugwiritsa ntchito adiresi ya ofesi ya nthambi.

  • Mungagwiritse ntchito dzina la munthuyo ngati mukulidziwa. Zimenezi zingathandize munthuyo kudziwa kuti kalatayo si yotsatsa malonda.

  • Mukamalemba kalatayo, yesetsani kulemba mawu molondola, kutsatira malamulo a chilankhulo komanso kugwiritsa ntchito moyenera zizindikiro za m’kalembedwe. Kalatayo iyenera kukhala yaukhondo. Ngati yalembedwa pamanja, zolemba zake ziyenera kukhala zowerengeka bwino. Mawu ake sayenera kukhala achibwana kapena aulemu wonyanyira.

Kalata yachitsanzoyi yalembedwa mogwirizana ndi mfundo zimenezi. Sikuti muyenera kungokopera ndendende m’mene yalembedwera. Mukhoza kusintha zina ndi zina kuti igwirizane ndi cholinga chanu, chikhalidwe komanso mmene zinthu zilili kwanuko.