Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​​—Muzilemba Makalata Abwino

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​​—Muzilemba Makalata Abwino

KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI? Buku la 1 Akorinto ndi limodzi mwa makalata 14 omwe Mtumwi Paulo analemba pofuna kulimbikitsa Akhristu anzake. Munthu akamalemba kalata amakhala ndi mwayi woganizira mawu omwe angagwiritse ntchito ndipo munthu wokaiwerengayo amakhala ndi mwayi woiwerenga mobwerezabwereza. Kulemba makalata ndi njira yabwino yolalikirira achibale komanso anzathu. Kumathandizanso polalikira anthu amene sitingakumane nawo mwachindunji. Mwachitsanzo, njirayi ingathandize anthu achidwi omwe tikulephera kuwapeza panyumba. Nthawi zina zimakhala zovuta kulalikira anthu ena a m’gawo lathu chifukwa amakhala m’nyumba zokhala ndi chitetezo chokhwima kwambiri, za m’mipanda komanso m’malo ovuta kufikako. Koma kodi tizikumbukira chiyani tikamalembera kalata munthu amene sitikumudziwa?

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

  • Lembani zimene mukanamuuza pamasom’pamaso. Kumayambiriro kwa kalatayo, fotokozani kuti ndinu ndani komanso cholinga chanu polemba kalatayo. Mungathenso kulemba funso loti munthuyo aliganizire n’kumuuza kuti akhoza kupeza yankho lake pawebusaiti yathu. Mukhozanso kumuuza za Phunziro la Baibulo la pa Intaneti, kapenanso kuti timaphunzira Baibulo ndi anthu ndipo mungamutchulire mitu ina ya m’mabuku amene timagwiritsa ntchito pophunzira ndi anthu. Potumiza kalatayo mungaikemonso khadi lodziwitsa anthu za jw.org kapena kapepala kalikonse

  • Musachulukitse zonena. Kalatayo isakhale yaitali moti munthu n’kufika potopa nayo.​—Onani kalata yachitsanzo

  • Mukamaliza, iwerengeni kuti mukonze molakwika komanso muone ngati ikumveka bwino. Kalatayo iyenera kukhala yowerengeka komanso yomveka mwaubwenzi. Muzionetsetsanso kuti mwaika masitampa okwanira chifukwa ngati pangakhale ndalama zotsala, munthu wokalandira kalatayo ndi amene angafunike kulipira