Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 1 AKORINTO 4-6

“Chofufumitsa Chaching’ono Chimafufumitsa Mtanda Wonse”

“Chofufumitsa Chaching’ono Chimafufumitsa Mtanda Wonse”

5:1, 2, 5-11, 13

Munthu akachotsedwa mumpingo zimakhala zopweteka kwambiri. Ndiye n’chifukwa chiyani tinganene kuti kuchita zimenezi kumasonyeza chikondi?

Tingatero chifukwa kuchotsa munthu . . .

  • kumasonyeza kuti timakonda Yehova chifukwa kumalemekeza dzina lake loyera.​—1 Pet. 1:15, 16

  • kumasonyeza kuti timakonda abale ndi alongo chifukwa kumawateteza kuti asatengere makhalidwe oipa.​—1 Akor. 5:6

  • kumasonyeza kuti timakonda wolakwayo chifukwa kumamuthandiza kuzindikira kulakwa kwake kuti alape.​—Aheb. 12:11

Kodi tingathandize bwanji Akhristu omwe ali ndi wachibale wochotsedwa?