Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | AROMA 12-14

Mmene Tingasonyezere Chikondi Chachikhristu

Mmene Tingasonyezere Chikondi Chachikhristu

12:10, 17-21

Munthu wina akatilakwira sitimangofunika kupewa kumuchitira zoipa. Koma ngati tili ndi chikondi chachikhristu, tidzamuchitirabe zinthu mokoma mtima. Baibulo limati: “Ngati mdani wako ali ndi njala, um’patse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, um’patse chakumwa. Pakuti mwa kutero udzamuunjikira makala a moto pamutu pake.” (Aroma 12:20) Zinthu zabwino zimene tingachitire munthu amene watilakwira zingathandize kuti munthuyo adzimvere chisoni n’kusintha.

Kodi munamva bwanji pamene munthu wina yemwe munamulakwira mosadziwa anakuchitirani zinthu mokoma mtima?