Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Tinganene

Zimene Tinganene

●○○ ULENDO WOYAMBA

Funso: Kodi cholinga cha Mulungu polenga anthu chinali chotani?

Lemba: Gen. 1:28

Funso la Ulendo Wotsatira: Kodi timadziwa bwanji kuti cholinga chomwe Mulungu analengera anthu chidzakwaniritsidwa?

○●○ ULENDO WOBWEREZA WOYAMBA

Funso: Kodi timadziwa bwanji kuti cholinga chomwe Mulungu analengera anthu chidzakwaniritsidwa?

Lemba: Yes. 55:11

Funso la Ulendo Wotsatira: Kodi moyo udzakhala wotani Mulungu akadzakwaniritsa cholinga chomwe analengera anthu?

○○● ULENDO WOBWEREZA WACHIWIRI

Funso: Kodi moyo udzakhala wotani Mulungu akadzakwaniritsa cholinga chomwe analengera anthu?

Lemba: Sal. 37:10, 11

Funso la Ulendo Wotsatira: Kodi tingatani kuti tidzalandire madalitso amene Mulungu analonjeza?

NTCHITO YOGAWIRA KAPEPALA KOITANIRA ANTHU KU CHIKUMBUTSO (March 23–April 19):

Tikukuitanani kumwambo wofunika kwambiri. Kapepala kanu ndi kameneka. Lachisanu pa 19 April, anthu mamiliyoni ambiri padziko lonse adzasonkhana kuti achite mwambo wokumbukira imfa ya Yesu Khristu. Kapepalaka kakusonyeza nthawi komanso malo omwe mwambowu udzachitikire m’dera lathu lino. Tikukuitananinso kuti mudzamvetsere nkhani ya mutu wakuti, “Yesetsani Kuti Mudzapeze Moyo Weniweni” yomwe idzakambidwe kutatsala mlungu umodzi kuti mwambowu uchitike.

Funso la Ulendo Wotsatira Ngati Munthuyo Wasonyeza Chidwi: N’chifukwa chiyani Yesu anafa?