March 16-22
GENESIS 25-26
Nyimbo Na. 18 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Esau Anagulitsa Ukulu Wake”: (10 min.)
Ge 25:27, 28—Esau ndi Yakobo anali ana amapasa koma anali ndi makhalidwe osiyana komanso ankakonda zosiyana (it-1 1242)
Ge 25:29, 30—Esau anachita zinthu mosaganiza bwino chifukwa cha njala komanso kutopa
Ge 25:31-34—Esau anagulitsa ukulu wake pousinthanitsa ndi chakudya chifukwa sankayamikira zinthu zopatulika (w19.02 16 ¶11; it-1 835)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Ge 25:31-34—Kodi nkhaniyi ikusonyeza bwanji kuti si nthawi zonse pamene mwana woyamba kubadwa ankakhala mumzere wa makolo a Mesiya? (Ahe 12:16; w17.12 15 ¶5-7)
Ge 26:7—N’chifukwa chiyani Isaki sananene zoona pa nthawi imeneyi? (it-2 245 ¶6)
Kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Ge 26:1-18 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo ya Ulendo Wobwereza Woyamba: (5 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi, kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: Kodi tingatani kuti tisamachititse manyazi mwininyumba ngati sakudziwa yankho la funso lomwe tamufunsa? Kodi wofalitsa wasonyeza bwanji luso pokambirana ndi mwininyumba lemba la Mateyu 20:28?
Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 4 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo wobwereza woyamba. (th phunziro 3)
Ulendo Wobwereza Woyamba: (Osapitirira 4 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza woyamba. Kenako m’patseni buku lakuti Zimene Baibulo Limaphunzitsa. (th phunziro 15)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzigwiritsa Ntchito Mavidiyo Pophunzira ndi Anthu Kabuku kakuti Uthenga Wabwino Wochokera kwa Mulungu: (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira? komanso yakuti N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Azivutika? Pambuyo poonera vidiyo iliyonse, kambiranani mafunso otsatirawa: Kodi mungagwiritse ntchito bwanji vidiyoyi mukamaphunzira ndi munthu kabuku ka Uthenga Wabwino? (mwb19.03 7) Kodi mwapeza mfundo zotani m’vidiyoyi zomwe zingakuthandizeni pophunzira ndi munthu? Kumbutsani ofalitsa kuti kabuku ka Uthenga Wabwino ka pazipangizo zamakono kali ndi malinki a mavidiyowa.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 77
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (Osapitirira 3 min.)
Nyimbo Na. 21 ndi Pemphero