March 30–April 5
GENESIS 29-30
Nyimbo Na. 93 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yakobo Anakwatira”: (10 min.)
Ge 29:18-20—Yakobo anavomereza kugwira ntchito kwa Labani kwa zaka 7 kuti akwatire Rakele (w03 10/15 29 ¶6)
Ge 29:21-26—Labani anapusitsa Yakobo pomupatsa Leya m’malo mwa Rakele (w07 10/1 8-9; it-2 341 ¶3)
Ge 29:27, 28—Yakobo sanalole kuti mavuto amene ankakumana nawo amufooketse
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Ge 30:3—N’chifukwa chiyani Rakele ankaona ana amene Yakobo anabereka ndi Biliha ngati ake? (it-1 50)
Ge 30:14, 15—N’chifukwa chiyani Rakele anataya mwayi wake woti akanatha kutenga pakati pousinthanitsa ndi mandereki? (w04 1/15 28 ¶7)
Kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Ge 30:1-21 (th phunziro 2)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kuwerenga Komanso Kuphunzitsa Mwaluso: (10 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo yakuti Kulankhula Molimbikitsa, kenako kambiranani phunziro 16 m’kabuku ka Kuphunzitsa.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 5 min.) bhs 59 ¶21-22 (th phunziro 18)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzilalikira Anthu Osaona”: (10 min.) Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Funsani omvetsera mafunso otsatirawa: N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tizilalikira anthu osaona? Kodi anthu osaona tingawapeze bwanji? Kodi tingasonyeze bwanji kuti timawaganizira tikamawalalikira? Kodi tili ndi zinthu ziti zomwe zingawathandize kuti akhale pa ubwenzi ndi Yehova?
Zimene Gulu Lathu Lachita: (5 min.) Onerani vidiyo ya Zimene Gulu Lathu Lachita ya March.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 79
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (Osapitirira 3 min.)
Nyimbo Na. 127 ndi Pemphero